Poem by Leornard Phiri from Mpondas CDSS CFT Club
Mpikisano woyenera pa malonda
Ndi m’nasi wakutsina phirikanilo
Wakuolotsa mbuna wakukonda
Tisawonjere deya mudiwa
Khani yalunjika pa malonda anuwo
Kaya ndinu ogulitsa ma sweet,
zimbwyende ndi mandasi
Musayese zida poti gulitsa malonda anu
Omwe anapanga expire
Mpikisano oyenera pa malonda
Tigulitseni zinthu zoyenera pa malonda
Mu nthawi yake
Chiyipira wachaje amake amati ndi mwana
Malonda anuwo musawaonele mubotolo
Mandasi, zigumu ndi ukadya ubwelele
Zomwezi lina tsiku mukafusa mtengo
Wa tayala la sienta
Mpikisano oyenera pa malonda
Tigulitseni malonda achilungamo
Osakhala za usizina mtole
Muwulawa unyolo
Ndipo mukapezeka mukugulitsa
Zinthu expire komanso zakuba
Mukwizingidwa komanso
Mufupa chosavina polipira
Chindapusa cha K500,000
Mpikisano oyenera pa malonda
Ogulitsa malonda inu
Mupewe nchitidwe oipa ngati
Kukhazikitsa mtengo umodzi pakati
Panu, Kubitsa kapena kuononga
Katundu ndi cholinga chofuna
Kukweza mtengo ndi kugulitsa zinthu
Zoopsya pa moyo, mukatelo
Malonda anu azakupindulilani
Mpikisano oyenera pa malonda
Tsono tadyani mutu pa samu
Imeneyi bola wanu mwana
Asalilire kuti adadi mukundimana
K30, 000 koma akuti ulipile
K500, 000 mayi Kalanga ine
Kupambana kuchiza kulewa
Ndipange dala anapita ndi madzi
Mpikisano oyenera pa malonda