Open your eyes kwacha tambala akalila kwacha
Eni malonda tiyeni tikapange ma kwacha
Musakonde tulo pakadafunda galu adajiwa
Malonda anuwo musawonjeze msuzi ayikeni
Poyera anthu aziwona okha musayike
Muthumba ngati malonda amphaka
Competition and Fair Trading Commission (CFTC)
Bwenzi lenileni kwa onse ochita
Malonda, iwowatu abwera ndi ulangizi ndi
Upangiri pa malonda anuwo
Malonda anuwo ogula ndi ogulitsa alindi
Ufulu okadandaula ku CFTC ngati
Wamenyedwa m’mimba likuswa mtengo
Malonda anuwo musawonjeza deya mudiwa
Wachiwona ndani bwanji muchepetse
Musachite zinthu mosokoneza dala poti
Mudzalapa atayeza mkhosi
Malonda anuwo musagulitse zinthu zomwe
Zidapanga expire chifukwa mudzawona
Ngati chauta wakondera atakukwidzingani
Palibe za ninvela apa pawawa
Ndipo pa malonda anuwo musabele anthu
Posemphanisa mitengo mwadala
Pangati chilungamo kuti zanu ziyende
Cholinga cha bungweli si kukubelani kapena kukuwopsyezani
Kapena kukubelani ayi koma chake cholinnga
Ndi chilungamo pa malonda, kuphunzita
Ndi kuziwitsa za ufulu wa ogula
Ndi ogulitsa kuti pasakhale chinyengo
Malonda anuwo ngati utsizina mtole udayendapo
Ndithu chanu chibalo cha sayizi yanu
Kuti mukaphunzire chilungamo pa malonda
Ndipo muzalipila lupiya lokwana K500, 000
Kapena kukagwira ntchito yakalavula gaga
Kwa dzilimika dzisano musadzati sindidanene
Za mpikisano oyenera pa malonda
Chofunika nkupanga chinvano cha mawu ngati amayi anvano
Ndi bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC)
Mudzamanga mansion ku mission
Ikakhala ntchezi idanva ndi liwu limodzi
Chikakhala chibweleza chidathetsa nkhunda
Kukhala nguluwe idakumbuka amake nsampha
Utaning’a